Psalms 113

1Tamandani Yehova.

Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
tamandani dzina la Yehova.
2Yehova atamandidwe,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake,
dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.

4Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse,
ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.
5Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,
Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?
6amene amawerama pansi kuyangʼana
miyamba ndi dziko lapansi?

7Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi
ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
8amawakhazika pamodzi ndi mafumu,
pamodzi ndi mafumu a anthu ake.
9Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake
monga mayi wa ana wosangalala.

Tamandani Yehova.
Copyright information for NyaCCL